Category

17 January, 2021

Nkhani Mchitumbuka

Malawi News Updates

Imwai ma Iron ngati magazi anu akuchepa mthupi

Kusowa magazi pamene muli oyembekezera

Pamene muli oyembekezera thupi lanu limasintha. Zina zochitika mthupi zimasiyana ndi mayi yemwe sali oyembekezera. Michere ina ya mthupi imafunika yochulukirapo, thupi limachotsa zoipa mochulukirapo komanso mumafunika magazi ochulukirapo kuposa amayi osayembekezera.

Mchere opangira magazi otchedwa Iron umafunika pafupifupi double (times 2) omwe mayi osayembekezera angafune patsiku.Ngati simukudya zakudya zokhala ndi iron okwanira mumatha kusowa magazi mthupi lanu.

Ndingadziwe bwanji kuti ndikusowa magazi pamene ndiri woyembekezera?

Ili ndi funso lofunikira kwambiri ndipo tiyeni tiliyankhe motere:

Pamene magazi akuchepa thupi lanu limakhala lofooka, manja ndi mapazi amazizira, kupuma mothamanga, thupi limaoneka lachikasu komanso kutupa kwa mapazi ndi malo ena.

Ngati mwalekerera nkuchedwa kupita Ku chipatala pamene muli oyembekezera mwana amatha kuzabadwa opanda thanzi komanso weight yochepa,kubeleka masiku asanakwane,mwana kumwalira akangobadwa komanso inuyo eni ake mumakhala pachipsezo chotaya moyo wanu komanso kuzadwala matenda a nkhawa mukabeleka mwa zina.

NDINGAPEWE BWANJI MATENDA OSOWA MAGAZI PAMENE NDILI OYEMBEKEZERA?

Mchere wa iron omwe umafunikira popanga magazi umafunika pafupi fupi 27mg patsiku pamene muli oyembekezera. Yesetsani kumadya zakudya za magulu onse makamaka zamasamba, nyama, nyemba zouma ndi nsomba.

Masiku ano mumayenera kumamwa mankhwala owonjezera magazi tsiku ndi tsiku. Pewani kunyalanyaza kumwa mankhwalawa. Ngati mukukumana ndi mavuto ena pankhani ya mankhwala fotokozerani akuchipatala.

Palinso mankhwala ena omwe mumakhala ma vitamin ambiri kuphatikizapo amagazi monga pegnatal, mom 2 be, pregnacare ndi ena ambiri omwe mutha kumamwa kuti thupi lanu lizikhala bwino.

Pitani ku sikelo mwandondomeko yake ndipo tsatirani malangizo onse omwe mwapatsidwa kuchipatala kuphatikizapo kumwa mankhwala oteteza matenda osiyanasiyana monga amagaziwa, a malungo ndi ena monga mmene akuchipatala akupatsirani kuti mupewe matenda ambiri. Izi zimathandiza uchembere wabwino komanso kuchepetsa imfa ya amayi.

Khalani a thanzi, kondani moyo wanu, tsatirani uchembere wabwino.