Category

17 January, 2021

Nkhani Mchitumbuka

Malawi News Updates

Kukwera kwa blood pressure

Kumvetsa vuto la kukwera kwa Blood Pressure (BP)

Vuto la kukwera kwa blood pressure si vuto lachilendo kwa anthu ambiri and masiku ano likupanga affect anthu ambiri.

Kukwera kwa BP ndikomwe kukuyambitsa matenda ena ambiri monga vuto la mtima, iphyo (kidney), stroke, matenda a maso komanso matenda ena ambiri. Izi zili choncho chifukwa nthawi zambiri munthu umangokhala osamadziwa kuti blood pressure yako ndiyokwera. That is why timapanga encourage anthu kupimisa pafupi pafupi

Kuti magazi ayende mmisempha ya mthupi pamafunika kugunda kwa mtima komanso space yabwino ya mu misempha kuti magazi aziyenda pa pressure (mphamvu) yoyenera. Ngati misempha yachepa in size kapena ngati mtima ukugunda mwa mphamvu kwambiri magazi amathamanganso ndi mphamvu. Titha kuyerekeza ndi horse pipe. Pamene munthu ukuyesera kuchepesa mpata wa katulukidwe ka madzi, madzi amatuluka amphamvu.

Now chilichonse chomwe chingapangise misempha kuchepa monga kuchepa kwa space ngakhalenso kuchuluka kwa fluid mu misempha kuphatikiza kupopa magazi mwa mphamvu kwa mtima, blood pressure imakwera.

Pamene BP yakwera mumatha kumva mutu kuwawa modabwitsa, kupuma mothamanga, kumva thupi kutentha modabwitsa,restlessness (kusowa mtendere) komano kutuluka magazi mphuno. Nthawi zina zizindikiro sizikhalapo.

Pali zambiri zomwe zimakweza blood pressure. Kudya za nchere ochuluka, kumwa mowa moonjeza, kusuta fodya, kukhala moyo osapanga ma exercise, kudya za mafuta ambiri, kukanika kupanga control weight yanu ndi zina zomwe zimachititsa BP kukwera.

Nthawi zina chifukwa cha matenda ena omwe mukudwala monga a kidney, mtima, kumwa mankhwala olera, thyroid disease and kukhala oyembekezera, mumathanso kukhala ndi vutoli. High blood pressure imathanso kupanga run through families (genetics).

Pamene makolo anu adwala blood pressure nanunso mumatha kukhala ndi increased risk.

Kupewa kudwala blood pressure nkupewa ZOPEWEKA pa zomwe ndakamba pamwambapa komanso kumapanga check pafupi pafupi blood pressure yanu. Mutha kugula ka machine ka digital nkumazipanga check pa family panu kuti mupewe kudwala matenda omwe amabwera ngati munthu ukhala ndi blood pressure yokwera kwa nthawi yaitali monga matenda a mtima komanso kuchepetsa chiopsezo chopanga stroke.

Pamene mukumwa mankhwala a BP imwani motsata malangizo. Masiku ano anthu akuchulutsa kudukiza mankhwalawa kapena kumangomwa ikakwera zomwe sizololedwa. Kumbukirani kuti nthawi zina munthu sudziwa kuti BP ikumakhala yokwera.

Refer on image for BP values