Category

23 September, 2020

Nkhani Mchitumbuka

Malawi News Updates

Anthu omwalira ndi Covid-19 sanati – Bambo Adamson

M'mbuyomu, atsogoleri ena mu boma la Kongeresi anayima pachulu ndikuliuza dziko kuti kuno kwathu ku Malawi kulibe Covid-19 akuterotu bambo Adamson

Bambo Adamson Muula yemwe ndi katswiri pa nkhani zokhuza umoyo wa anthu mdziko muno, wachenjeza kuti dziko la Malawi likupita kuchionongeko komwe anthu omwalira ndi Covid-19 ayambe kuchuluka tsiku ndi tsiku.


Iye wati anthu ayembekezere zotsatira zowopsa kwambiri mwezi ukubwerawu.

Pakadali pano mulili wa Covid-19, wafika povuta kwambiri mdziko muno ndipo tsiku ndi tsiku tikutaya abale ndi abwezi chifukwa cha muliliwu.

Boma lomwe lilipo pano, ndilomangika kuchitapo kanthu chifukwa cha manyazi popeza zina mwanjira zopewela muliliwu iwo adazisusapo mbuyomu pomwe anali kunja kwa boma.
Ichi ndi chifukwa chake muliliwu wafika poyipa kwambiri.
.
M’mbuyomu, atsogoleri ena mu boma la Kongeresi anayima pachulu ndikuliuza dziko kuti kuno kwathu ku Malawi kulibe Covid-19

Izi zaonjezera kuyika miyoyo ya a Malawi ambiri pa mavuto.

Ndi Nkhani Mchittumbuka simudzakhalanso mu mdima wa chilungamo.